LACHIWIRI LAMULUNGU WA 21 PACHAKA// 26 AUGUST 2025//FR JOHN KALIWAMBA DP

TIYANKHULENI AMBUYE 26 AUGUST, 2025 LACHIWIRI LAMULUNGU WA 21 MU NYENGO YAPACHAKA MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YOYAMBA YA PAULO KWA ATESALONIKA 2:1-8 Abale, inu nomwe mukudziŵa kuti kucheza kuja tidadzacheza kwanuku, kudali kwaphindu. Monga mukudziŵa, paja nthaŵi imene ija nkuti anthu aku Filipi atatizunza kale ndi kutichita chipongwe. Komabe Mulungu wathu adatilimbitsa mtima mpaka tidakulalikirani ndithu Uthenga wake Wabwino, ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti zimene timalalika sitizilalika chifukwa chofuna kuphunzitsa zonama, kapena kuganiza zoipa, kapena kufuna kunamiza anthu ayi. Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungitsa Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu. Monga mukudziŵa, sitidabwere kwanuko ndi mawu oshashalika kapena ndi mtima womangofuna phindu. Apo Mulungu angathe kutichitira umboni. Sitinkafunanso ulemu wochokera kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, ngakhale kudali kotheka kukulamulani kuti mutithandize, popeza kuti ndife Atumwi a Khristu. Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mayi wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 139: 1-3, 4-6 Chauta Mulungu wanga, mwandifufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa (1). Chauta, mwandifufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, Mumazindikira maganizo anga mudakali kutali. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, Mumadziŵa njira zanga zonse. *Chauta Mulungu wanga, mwandifufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa*. Ngakhale mawu anga asadafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse. Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo, Ndipo mumandisanjika dzanja lanu. Nzeru zimenezi nzopitirira nzeru zanga, Nzapamwamba, sindingathe kuzimvetsa. *Chauta Mulungu wanga, mwandifufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa*. *Aleluya*: (_Ntchito 16: 14_) Atate, tsekulani mitima yathu kuti tilandire Mawu a Mwana wanu, Yesu Khristu, *Aleluya*. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MATEYU WOYERA 23:23-26 Yesu adati: “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka cha chikhumi cha timbewu tonunkhira, ndi cha timbewu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Inu atsogoleri akhungu, mumakuntha zakumwa zanu kuti muchotsemo kanchenche, koma mumameza ngamira. Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale, koma mkati mwake ndi modzaza ndi nzeru za kuba, ndi za umbombo. Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka mkati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera.” Mthenga wa Ambuye

LOLEMBA LAMULUNGU WA 21 PACHAKA ||25 AUGUST 2025|| FR JOHN ENOCH KALIWAMBA DP
▶︎

LOLEMBA LAMULUNGU WA 21 PACHAKA ||25 AUGUST 2025|| FR JOHN ENOCH KALIWAMBA DP

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE
▶︎

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE

Pakaipa! Mai Vakauraya Mwana Nenguruve (Full Story) Ngezi's court | Chibanda media
▶︎

Pakaipa! Mai Vakauraya Mwana Nenguruve (Full Story) Ngezi's court | Chibanda media

ZOMWE APANGA ATSILIKALI KWA NSUNDWE ~KOMA ZOONA ANGAPANGE KHALIDWE ILI
▶︎

ZOMWE APANGA ATSILIKALI KWA NSUNDWE ~KOMA ZOONA ANGAPANGE KHALIDWE ILI

UMBONI WA PASTOR EFRAIME GIBSON AMENE ANAFA NDIKUUKASO KUTI ADZACHITILE UMBONI DZINA LA YESU
▶︎

UMBONI WA PASTOR EFRAIME GIBSON AMENE ANAFA NDIKUUKASO KUTI ADZACHITILE UMBONI DZINA LA YESU

Apostle Chiwenga's Shocking Prophecy About Zimbabwe's Next Coup
▶︎

Apostle Chiwenga's Shocking Prophecy About Zimbabwe's Next Coup

LOWERUKA LAMULUNGU WA 21 PACHAKA//30 AUGUST 2015// FR KALIWAMBA JOHN
▶︎

LOWERUKA LAMULUNGU WA 21 PACHAKA//30 AUGUST 2015// FR KALIWAMBA JOHN

Ambassadors Of Christ Choir Songs Playlist.#ambassadorsofchristchoirrwanda #jesus #christianmusic
▶︎

Ambassadors Of Christ Choir Songs Playlist.#ambassadorsofchristchoirrwanda #jesus #christianmusic

LACHINAI KUTSATIRA PHULUSA//19 FEBRUARY 2026// FR FRANCIS DAMASEKE DP
▶︎

LACHINAI KUTSATIRA PHULUSA//19 FEBRUARY 2026// FR FRANCIS DAMASEKE DP

LAMULUNGU WA 5 WA LENT|| 22 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE DP
▶︎

LAMULUNGU WA 5 WA LENT|| 22 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE DP

Mukifo kiri , Kampumulire, Number one , mpulira yesu , kino kyennasigaza eno kunsi
▶︎

Mukifo kiri , Kampumulire, Number one , mpulira yesu , kino kyennasigaza eno kunsi

Shocking Prophecy for Zimbabwe pazoshata manje chiporofita icho chazadziswa
▶︎

Shocking Prophecy for Zimbabwe pazoshata manje chiporofita icho chazadziswa

Musachedwe ndikuwalingalila, ayandikileni mudziwe || Rev. Y. Gama
▶︎

Musachedwe ndikuwalingalila, ayandikileni mudziwe || Rev. Y. Gama

LOLEMBA LAMULUNGU WA 5 WA LENT//23 MARCH 2026/ FR ELIZEO NTHALIKA DP
▶︎

LOLEMBA LAMULUNGU WA 5 WA LENT//23 MARCH 2026/ FR ELIZEO NTHALIKA DP

CHIWANDA CHIKAGWIRA MUNTHU ,UMASILIRA NAMALIRA
▶︎

CHIWANDA CHIKAGWIRA MUNTHU ,UMASILIRA NAMALIRA

Mukadzi Mushunemi by Evangelist Muparinga at United Methodist Church Murehwa
▶︎

Mukadzi Mushunemi by Evangelist Muparinga at United Methodist Church Murehwa

Omwoyo Deep Woesip Nonstop  Pr  John Muyizzi  Preaching Gospel to all nations
▶︎

Omwoyo Deep Woesip Nonstop Pr John Muyizzi Preaching Gospel to all nations

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 4 WA LENT||17 MARCH 2026|| FRANCIS FR DAMASEKE DP
▶︎

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 4 WA LENT||17 MARCH 2026|| FRANCIS FR DAMASEKE DP

Piliranibe kufikira chimaliziro - by Pr. BL Mbewe
▶︎

Piliranibe kufikira chimaliziro - by Pr. BL Mbewe

LACHISANU LAMULUNGU WA 3 WA LENT|| 13 MARCH 2026|| FR JOHN KALIWAMBA DP
▶︎

LACHISANU LAMULUNGU WA 3 WA LENT|| 13 MARCH 2026|| FR JOHN KALIWAMBA DP