LOLEMBA LAMULUNGU WA 21 PACHAKA ||25 AUGUST 2025|| FR JOHN ENOCH KALIWAMBA DP
TIYANKHULENI AMBUYE 25 AUGUST, 2025 LOLEMBA LAMULUNGU WA 21 MU NYENGO YAPACHAKA MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YOYAMBA YA PAULO KWA ATESALONIKA 1:1-5,8b-10 Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Tikulembera Mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kumakutchulani m’mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m’mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m’mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m’mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu. Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziŵa kuti Iye adakusankhani kuti mukhale ake. Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sudali wa pakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m’mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni. Ndipo kuwonjezera apo, mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu, idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu. Iwo amakamba okha za m’mene mudatilandirira, ndi za m’mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira. Tsopano mukudikira Mwana wake kuti abwerenso kuchokera Kumwamba. Mwana wakeyo ndi Yesu, amene Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ulikudza. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 149: 1B-2, 3-4, 5-6A NDI 9B Chauta Mulungu wathu amakondwera ndi anthu ake (4a). Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda Pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Aisraele asangalale ndi Mlengi wawo. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo. *Chauta Mulungu wathu amakondwera ndi anthu ake*. Atamande dzina lake povina, Amuimbire nyimbo yokoma ndi ng’oma ndi pangwe. Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, Amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani awo. *Chauta Mulungu wathu amakondwera ndi anthu ake*. Okhulupirika akondwerere kugonjetsa kopambanaku, Aziyimba mokondwa ali gone pa mabedi. Atamande Mulungu kwambiri mokweza mawu, Uwu ndiwo ulemerero wa anthu okhulupirira Chauta. *Chauta Mulungu wathu amakondwera ndi anthu ake*. *Aleluya*: (_Yohane 17: 17_) Mawu anu ngoona kopambana, ndipo muŵapatule anthu ndi mawu anu kuti onse akhale anuanu, *Aleluya*. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MATEYU WOYERA 23:13-22 Yesu adati kwa gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake: “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatseka pakhomo pa Ufumu wa Kumwamba kuti anthu asaloŵemo. Paja inu nomwe simuloŵamo, ndipo mumatsekereza amene amafuna kuloŵamo. Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera chuma akazi amasiye, kwinaku nkumanyengezera kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa. Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumayenda maulendo ambirimbiri pa nyanja ndi pa mtunda, kufunafuna ngakhale munthu mmodzi yekha kuti atembenuke ndi kusanduka wophunzira wanu. Tsono akapezeka, mumamsandutsa woyenera kulangidwa ku Jehena kuposa inu kaŵiri. Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati: ‘Munthu akalumbira kuti: Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti: Pali chuma cha m’Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’ Inu anthu opusa ndi akhungu! Chachikulu nchiti, chuma chija, kapena Nyumba imene ikusandutsa chumacho kuti chikhale chopatulika? Mumatinso: ‘Munthu akalumbira kuti: Pali guwa la nsembe, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti: Pali choperekedwa pa guwa, asunge lumbiro lakelo.’ Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa la nsembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika? Tsonotu munthu akalumbira kuti: Pali guwa la nsembe, walumbiranso pa zonse zimene zili pa guwapo. Akalumbira kuti: Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m’Nyumbamo. Ndipo akalumbira kuti: Kumwambadi, walumbiranso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndiponso pa Iye amene amakhala pa mpandopo.” Mthenga wa Ambuye

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE

''WUMI WEYI WUNOOKI MUKUWUNDA'' (May Your Soul Rest in peace)

The Sad Story of Cameroon | PLO Lumumba Exposes Hidden Truths

What Nigerian Officials Told Stranded Citizens In South Africa Got Everyone Angry

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 21 PACHAKA// 26 AUGUST 2025//FR JOHN KALIWAMBA DP

UMBONI WA PASTOR EFRAIME GIBSON AMENE ANAFA NDIKUUKASO KUTI ADZACHITILE UMBONI DZINA LA YESU

Why Land Is Going To Be Museveni's Last War || The Morning After With Joseph Kabuleta Episode 11

How Noah's Ark Was Designed — Biblical Engineering

ZOMWE APANGA ATSILIKALI KWA NSUNDWE ~KOMA ZOONA ANGAPANGE KHALIDWE ILI

CHIWANDA CHIKAGWIRA MUNTHU ,UMASILIRA NAMALIRA

LAMULUNGU WA 5 WA LENT|| 22 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE DP

CHIHANA WAUZIDWA IZI KUCHA KWA LERO ~ZACHIZIWIKIRE AZIKAKONZA CHIPANI CHAKE

JESUS Appeared in My Dream and Warned Me About This | Julius Malema Story

PLO Lumumba BLASTS South Africa: "This Is Not Xenophobia, It's Afrophobia"

The Spirit of Adoration by Rev Fr Enoch Kanjira

IMANA IYO IRAMBUYE UKUBOKO KWAYO IMIYAGA N'IMIRABA BIRAHUNGA /// Paster Antoine RUTAYISIRE

John Lennox Brilliant Response on "Why did God command Killing in the Bible?"

Evangelist Muparinga Preaching at a funeral

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 4 WA LENT||17 MARCH 2026|| FRANCIS FR DAMASEKE DP

