Tili ndi iwe – by The QFM

Zilipo nthawi zimene aliyense amasowa abwenzi ndi abale ocheza nawo ndi olimbikitsana nawo mu nthawi zimene tikukumana ndi zovuta zosiyanasiyana za mmoyo uno... Izi ndi nthawi zimene mtima umachita kumva kuti chinachake pa iwe chikusowekera... Mulungu anachiika chimenechi mu zolengedwa zake zonse (Aroma 14:7) Choteronso Yesu mu Getsemani anasowekera chilimbikitso kuchokera kwa ophuzira Ake omwe... (Olimbikitsa anzakeyo, anafunikiranso chilimbikitso!, Nkuona kawiri-konse anapemphera kuti "chikhocho chimudutse!") Yesu, podutsa mu Getsemani, ndi yekhayo mu Zakumwamba, amene angamvetsetse modzadza za kufunikira kolimbitsana mitima mu moyo umene tikukhalawu, umene Satana amabweretsa zoofooketsa zambiri kuti anthu a Mwiniwake-fe tisakhalenacho chiyembekezo ndi chilimbikitso chokomacho, chomwe Ambuye wathu Yesu anachionetsera pamtanda ndi kuyambira pachiyambi pomwe! Potero musaope, kumwamba kukuti: "Tili ndi iwe!"