David Kanyenda: Kunalibe Reaserch department ku Manoma!

Mupulogalamu ya Pampani lero tikumaliza kualankhula ndi a David Kanyenda omwe ndi katswiri wa za malamulo komanso m’modzi wa akuluakulu a timu ya Mighty Wanderers. Lero a Kanyenda alankhulapo pa zomwe Bungwe la FAM lachita pokhazikitsa bungwe lowunika mikangano la National Dispute Resolution Chamber, Zokhudza ntchito yoteteza ukatswiri wa Super League ndi zina zambiri. Khalani pompo ndi kuwonera usiku uno kuyambira nthawi ya 9:00 PM