IMFA YA YOHANE MBATIZI//29 AUGUST 2025// FR JOHN KALIWAMBA

TIYANKHULENI AMBUYE 29 AUGUST 2025 IMFA YA YOHANE MBATIZI MAWU OYAMBA, A MBUKU LA MNENERI YEREMIYA 1:17-19 Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukaŵauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuwona. Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 71: 1-2,3-4a, 5-6ab,15ab ndi 17 Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu, Inu Chauta Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta. Musandichititse manyazi. Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa, pakuti ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse. Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu, Inu Chauta Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Landitseni Inu Mulungu wanga kwa anthu oipa, landitseni ku mphamvu za anthu osalungama ndi ankhalwe. Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu, Inu Chauta Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga. Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu, Inu Chauta Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. *Aleluya*: (Mat 5:10) Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao, *Aleluya*. MTHENGA WABWINO WA MARKO 6:17-29 _Ndifuna kuti tsopano pompano mundipatse mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale_. Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Ndiye kuti Herode anali atamkwatira maiyo. Ndipo Yohane adaamuuza kuti, “Nkulakwira Malamulo kulanda mkazi wa mbale wanu.” Tsono Herodiasiyo ankadana naye Yohane, ndipo ankafuna kuti aphedwe basi. Koma ankalephera, chifukwa Herode ankaopa Yohane, podziŵa kuti anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Choncho ankamusunga bwino. Ankakonda kumamvetsera mau ake, ngakhale kuti akamumva choncho, ankathedwa nzeru. Koma pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, Herodiasi adapezerapo mwai. Herodeyo adakonza phwando, naitana akuluakulu a Boma, ndi akulu olamulira asilikali, ndi anthu omveka a ku Galileyako. Tsono mwana wamkazi wa Herodiasi adaloŵa, nayamba kuvina. Kuvinako adakondweretsa nako kwambiri Herode ndi amene adaali naye paphwandopo. Pamenepo mfumuyo idauza mtsikanayo kuti, “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna, ine ndikupatsa.” Ndipo adatsimikiza molumbira kuti, “Chilichonse chomwe uti undipemphe, ndikupatsa ndithu, ngakhale kukudulira dziko langa lino pakati.” Mtsikanayo adatuluka nakafunsa mai wake kuti, “Kodi ndikapemphe chiyani?” Mai wakeyo adati “Kapemphe mutu wa Yohane Mbatizi.” Mtsikana uja adabwerera msanga kwa mfumu nanena kuti, “Ndifuna kuti tsopano pompano mundipatse mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.” Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni kwambiri. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, sadafune kuphwanya lonjezo lake kwa mtsikanayo. Choncho nthaŵi yomweyo adatuma mmodzi mwa asilikali ake, namulamula kuti abwere nawo mutu wa Yohanewo. Msilikaliyo adapita ku ndende, nakamdula mutu Yohaneyo. Adaika mutu wakewo m'mbale nkubwera nawo, naupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake. Ophunzira a Yohane atamva zimenezi, adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Mthenga wa Ambuye

LOWERUKA LAMULUNGU WA 4 WA LENT|| 21 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE
▶︎

LOWERUKA LAMULUNGU WA 4 WA LENT|| 21 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE

Shocking Prophecy for Zimbabwe president ED forced to resign hazvina kumira mushe
▶︎

Shocking Prophecy for Zimbabwe president ED forced to resign hazvina kumira mushe

Karen Through The Bible 1 Samuel 6:13 - 8:18
▶︎

Karen Through The Bible 1 Samuel 6:13 - 8:18

Abatwa nemukadzi wemunhu wachitoita bonde
▶︎

Abatwa nemukadzi wemunhu wachitoita bonde

Uchabe wakuyang'ana mmbuyo-Fr Elizeo Nthalika
▶︎

Uchabe wakuyang'ana mmbuyo-Fr Elizeo Nthalika

Imvani momwe satana tingamugonjetsere
▶︎

Imvani momwe satana tingamugonjetsere

Mukadzi Mushunemi by Evangelist Muparinga at United Methodist Church Murehwa
▶︎

Mukadzi Mushunemi by Evangelist Muparinga at United Methodist Church Murehwa

La vida de Jesús | Español | Life of Jesus (Gospel of John) Official Spanish Full HD Movie (HD)
▶︎

La vida de Jesús | Español | Life of Jesus (Gospel of John) Official Spanish Full HD Movie (HD)

23RD SUNDAY OF ADVENT || 9 SEPTEMBER 2025 || FR FRANCIS DAMASEKE DP
▶︎

23RD SUNDAY OF ADVENT || 9 SEPTEMBER 2025 || FR FRANCIS DAMASEKE DP

Omwoyo Deep Woesip Nonstop  Pr  John Muyizzi  Preaching Gospel to all nations
▶︎

Omwoyo Deep Woesip Nonstop Pr John Muyizzi Preaching Gospel to all nations

Mudzimai wenyu haana kuenda kuMoza ari kuchikomba chake/prophet miracle paul
▶︎

Mudzimai wenyu haana kuenda kuMoza ari kuchikomba chake/prophet miracle paul

LACHISANU LAMULUNGU WA 3 WA LENT|| 13 MARCH 2026|| FR JOHN KALIWAMBA DP
▶︎

LACHISANU LAMULUNGU WA 3 WA LENT|| 13 MARCH 2026|| FR JOHN KALIWAMBA DP

Evangelist T. Muparinga - Urikuonei? at AFM Midlands Conference
▶︎

Evangelist T. Muparinga - Urikuonei? at AFM Midlands Conference

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE
▶︎

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE

CHIWANDA CHIKAGWIRA MUNTHU ,UMASILIRA NAMALIRA
▶︎

CHIWANDA CHIKAGWIRA MUNTHU ,UMASILIRA NAMALIRA

LACHISANU LAMULUNGU WA 23 PACHAKA || 12 SEPTEMBER 2025|| FR FRANCIS DAMASEKE DP
▶︎

LACHISANU LAMULUNGU WA 23 PACHAKA || 12 SEPTEMBER 2025|| FR FRANCIS DAMASEKE DP

Amai tokutsemurai here kana kuti mozvitsemura/Prophet miracle paul
▶︎

Amai tokutsemurai here kana kuti mozvitsemura/Prophet miracle paul

3.Ibihe byo kwa Nowa , Igishushanyo mbonera cyo kugaruka kwa Yesu By HABINEZA Jean Claude
▶︎

3.Ibihe byo kwa Nowa , Igishushanyo mbonera cyo kugaruka kwa Yesu By HABINEZA Jean Claude

MAPHUNZIRO A PADERA A NYENGO YA LENT || DAY 19|| 11 MARCH 2026|| FR FRANK PHIRI DP
▶︎

MAPHUNZIRO A PADERA A NYENGO YA LENT || DAY 19|| 11 MARCH 2026|| FR FRANK PHIRI DP

WAUMINI WABAKI HOI KANISANI/PADRE MWENYE KIPAJI NA KARAMA YA AJABU/SHUHUDIA ALICHOKIFANYA''SAMEHE''
▶︎

WAUMINI WABAKI HOI KANISANI/PADRE MWENYE KIPAJI NA KARAMA YA AJABU/SHUHUDIA ALICHOKIFANYA''SAMEHE''