Khalabe Odikira - The Morning Star (Official Video)

Lyrics: 1. Zosautsa zochuluka okondedwa m'moyowu Kukumana ndi zipsinjo zosaneneka Kuyesetsa kupemphera ngati Mlungu saakumva Zafika povuta moyuwu kuwawa Kuyang’ana uko wachoka ndizogwetsa mphwayi Kuganiza zatsogolo mtima umasweka Nthawi zina ukaona ena zithu zikuwayendera Zimangopangitsa ‘we kukhumudwa Chorus Kaya nyengo ivute iwopse bwanji Ndi zinthu za kanthawi kanthawi kochepa Zisakuchotse ‘we pamaso pa Mulengi wako Khalabe odikira mkhulupire Akulonjeza kukhala nawe kukusamalira zinthu zikavuta Ngakhale lonjezano lake lichedwe bwanji Khalabe odikira mkhulupire 2. Zolilitsa tsiku ndi tsiku kuopsedwa m'moyowu Kunyozedwa ndiopembedza nao limodzi Komabe m'nyengo zotere kumbuka liripo bwenzi Bwenzi lopambana ndiye Yesu Akhala nawe poyenda akhala nawe pogona Akhala mawe mtendere ndinso polira Iye ali ndi chinsisi cha tsogolo la moyo wako Khalabe odikira mkhulupire ----------------------------------------------------- The Morning Star, Kawale, Lilongwe Audio by: Recall, Kuimba Mwamphamvu Studio Video by: Hope Channel Malawi ----------------------------------------------------- Share this video:    • Khalabe Odikira - The Morning Star (Offici...   Subscribe for more videos:    / @themorningstar-mw   Audio playlist:    • M'bandakucha Album - The Morning Star   ----------------------------------------------------- Connect with us: Facebook:   / themorningstarsingersmw   Instagram:   / themorningstar_mw   Whatsapp: https://whatsapp.com/channel/0029Va5V... Spotify - https://spotify.link/EC6GyW0v3xb E-mail: [email protected]