CHAKA CHAKULEMEKEZA MTANDA| 14 SEPTEMBER 2025| FR FRANCIS DAMASEKE DP
TIYANKHULENI AMBUYE 14 SEPTEMBER 2025 TSIKU LOLEMEKEZA MTANDA WOYERA MAU OYAMBA; A MBUKU LA NUMERI 21:4b-9 Panthawi imeneyo: Aisraele adayamba kunyong'onyeka. Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.” Tsono Chauta adatumiza njoka za ululu wonga moto pakati pa anthu aja, ndipo zidaŵaluma, kotero kuti Aisraele ambiri adafa. Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange njoka yamkuŵa, ndipo uipachike pa mtengo. Aliyense wolumidwa akangoiyang'ana njokayo, adzakhala moyo.” Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 78: 1-2,-34-35,36-37,38 Musaiwale Ntchito Zomwe Chauta adachita Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani, inu anthu anga. Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga. Ndidzakusimbirani fanizo. Ndidzalankhula nkhani zobisika zakalekale, Musaiwale Ntchito Zomwe Chauta adachita Pamene ankapha ena, otsalira ankayamba kumufunafuna. Ankalapa namafunafuna Mulungu ndi mtima wao wonse. Adakumbukira kuti Mulungu ndi thanthwe loŵateteza, Musaiwale Ntchito Zomwe Chauta adachita Koma iwo adamthyasika ndi pakamwa pao, adamnamiza ndi lilime lao. Mtima wao sunali wokhulupirika kwa Iye. Sadasunge chipangano chake. Musaiwale Ntchito Zomwe Chauta adachita Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake. Kapena (Angathe kuwerengedwa ngati Mau Achiwiri MAWU A MKALATA YA PAULO KWA AFILIPI 2:6-11 Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Mau a Ambuye ALELUYA Tikupembedzani Amuye Yesu ndi kuyamika Inu, chifukwa mudaombola dziko lonse ndi Mtanda wanu ALELUYA MTHENGA WABWINO WA YOHANE 3: 13-17 Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba. “Monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m'chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa, kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye. Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse. Mthenga wa Ambuye

LAMULUNGU WA 5 WA LENT|| 22 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE DP

ZOMWE WAYANKHURA NJAWALA CHAKWERA AKOMOKA NDI BP~ CHAKWERA ANAPANGIRANJI KOMA

Apostle Chiwenga's Shocking Prophecy About Zimbabwe's Next Coup

Satana asadzakunamizeni

UMBONI WA PASTOR EFRAIME GIBSON AMENE ANAFA NDIKUUKASO KUTI ADZACHITILE UMBONI DZINA LA YESU

Goodness of God ✝️ Hillsong-Style Worship | Best Praise & Worship Songs Playlist 2026

Mukadzi Mushunemi by Evangelist Muparinga at United Methodist Church Murehwa

CAN BRIAN MUNDUBILE BE TRUSTED TO RUN THE COUNTRY?

KULEMEKEZA YOSEFE WOYERA MWAMUNA WA MARIA|| 19 MARCH 2026|| FR FRANCIS DAMASEKE

ZOMWE APANGA ATSILIKALI KWA NSUNDWE ~KOMA ZOONA ANGAPANGE KHALIDWE ILI

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 4 WA LENT||17 MARCH 2026|| FRANCIS FR DAMASEKE DP

CHISALE NDIYEMWE ANATUMIDWA KUTI APANGE IZI | KWASALAKU CHAKWERA AFERA MANJA MWA CHISALE

Musachedwe ndikuwalingalila, ayandikileni mudziwe || Rev. Y. Gama

Worship Music 2026 ✝️ | Nonstop Christian Praise & Worship Songs Playlist

The Spirit of Adoration by Rev Fr Enoch Kanjira

Evangelist Muparinga Preaching at a funeral

LOLEMBA LAMULUNGU WA 5 WA LENT//23 MARCH 2026/ FR ELIZEO NTHALIKA DP

USHUHUDA:KWA NINI MWINJ.MICHAEL MALAGILA AMEJITENGA NA MFUMO WA SDA GENERAL CONFERENCE.//0752925592

MAPHUNZIRO APADERA A LENT|| DAY 18|| 10 MARCH2026|| FR FRANK PHIRI

