CRUISE 5 WITH PROFESSOR YUSUF JUWAYEYI - ARCHEOLOGIST
Professor Yusuf Juwayeyi akugwila ntchito ku America ku Long Island University, Brooklyn komwe adayamba ntchito mu 2002. A Juwayeyi ndi katswiri ofufuza za mbiri ya anthu ndi nyama, pachingelezi Archeologist. Iwo afufuza zambiri mdziko la Malawi komanso kunja – ntchito yomwe imakhudza kukumba pansi kuti apeze mafupa aanthu ndi nyama zakalekale, komanso ziwiya zawo kuti amvetse mmene zinthu zinkakhalira kalelo. Pano a Juwayeyi alemba buku lotchedwa Archaeology and Oral Tradition in Malawi: Origins and Early History of the Chewa. Bukuli likukamba za mbiri ya aChewa, kumene adachokera, kumene adafikila kuno ku Malawi komanso makhalidwe awo amakedzana. Iwo akuti adafukula mafupa a aChewa amene adakhala ku Mankhamba. Akuti adapeza umboni wakuti aChewa anthawiyo anali achuma kwambiri ndi zina zopatsa chidwi zomwe alemba mu bukuli. Professor Yusuf Juwayeyi adabadwa ndikukulira ku Malawi. Aphunzitsako ku Chancellor College, Hunter College ya City University yaku New York komanso ngati oyesa mayeso a Archaeology ku University of Dar-es-Salaam ku Tanzania mu 1993. Anagwilako mboma ku Malawi ku Department of Antiquities mu 1989 kenako ngati Commissioner for Culture mu 1992. Mchaka cha 2000 anasankhidwa kukakhala kazembe wadziko la Malawi ku United Nations ku New York.

CRUISE 5 WITH DR STANLEY KHAILA PART 2

| CRUISE 5 WITH DR ALEX BANDA

Llamas: Reported June 12 rally fizzles out amid lack of trigger | Morning Matters

How Africa got a messed up education system - Prof Plo Lumumba explains

Archaeology and Oral Tradition in #Malawi. Prof Juwayeyi at The Culture Lab

CRUISE 5 WITH DR STANLEY KHAILA PART 1

Cruise 5 with Chrisford Chalera - Mouth Painter

CRUISE 5: ndi Frank Joab chakhaza

CRUISE 5 - CHIFUNO CHIFUNDO MLAMBE - CHIPEMBEDZO CHAMAKOLO ACHIKUDA

KUTUKULA ULIMI M'MALAWI...epi 22

CRUISE 5 WITH BYSON KAULA - DEATH ROW SURVIVOR

Professor John Chisi Reveals What Really Happened Inside Tonse Alliance |EP 041| Face 2 Face Podcast

ZodiakTV | CRUISE 5 WITH BURNING SPEAR

Igbo-Ukwu Mysteries: Historian’s Shocking 1990 Speech at the International Igbo Conference

CRUISE 5 WITH PETER DIMBA

CRUISE 5 WITH ULADI MUSSA

CRUISE 5 WITH DR. DONALD KAMDONYO

CRUISE 5 WITH APOSTLE STANLEY SELBY NDOVIE FOUNDER LIVING WATERS CHURCH

CRUISE 5 ON MBENJE ISLAND SALIMA 13 NOVEMBER 2022

