Umboni wa Mayi Mawindo - za Gahena ndi Paradaizo

Nawu umboni wa Mayi Mawindo womwe adaupereka pa wailesi ya FM 101. Mu umboniwu, akufotokoza za Gahena komanso Paradaizo. Ku Mateyu 13:42, Ambuye Yesu akufotokoza za ng'anjo ya moto momwe anthu onse ochimwa adzaponyedwe "kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano." Verse ya 43 ikupitilira motere: "Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve."